Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 61:7 - Buku Lopatulika

7 Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu; mumpatse chifundo ndi choonadi zimsunge.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu; mumpatse chifundo ndi choonadi zimsunge.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Akhale pa mpando wake waufumu pamaso pa Mulungu mpaka muyaya. Inu Chauta, mumsunge mokhulupirika chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya; ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 61:7
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.


sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.


Ndipo dzina lanu likulitsidwe ku nthawi zonse, kuti Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele, ndi nyumba ya mnyamata wanu Davide idzakhazikika pamaso panu.


Ulemerero wake ngwaukulu mwa chipulumutso chanu; mumchitira iye ulemu ndi ukulu.


Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.


Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.


Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere; zindifikitse kuphiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.


Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.


Chifundo ndi ntheradi zisunga mfumu; chifundo chichirikiza mpando wake.


Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.


ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo kunthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.


Pakuti Khristu sanalowe m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu mu Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa