Masalimo 128 - Buku LopatulikaWakuopa Yehova adalitsidwa m'banja mwake Nyimbo yokwerera. 1 Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake. 2 Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera. 3 Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako. 4 Taonani, m'mwemo adzadalitsika munthu wakuopa Yehova. 5 Yehova adzakudalitsa ali mu Ziyoni; ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako. 6 Inde, udzaona zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israele. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi