Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 128:1 - Buku Lopatulika

1 Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 128:1
24 Mawu Ofanana  

Pakuti ndinasunga njira za Yehova, osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga.


Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.


Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.


Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;


Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.


Adzadalitsa iwo akuopa Yehova, aang'ono ndi aakulu.


Odala angwiro m'mayendedwe ao, akuyenda m'chilamulo cha Yehova.


inde, sachita chosalungama; ayenda m'njira zake.


Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.


Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?


Ndinakondwera m'mene ananena nane, Tiyeni kunyumba ya Yehova.


Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba.


Akadapanda kukhala nafe Yehova, anene tsono Israele;


Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.


Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota.


Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.


Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.


Ha! Akadandimvera anthu anga, akadayenda m'njira zanga Israele!


Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo pa iwo amene amuopa Iye.


Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


Pamenepo ndipo Mpingo wa mu Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.


Mudzakhala odala m'mzinda, ndi odala kubwalo.


Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa