Masalimo 128 - Mawu a Mulungu mu Chichewa ChaleroSalimo 128 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake. 2 Udzadya chipatso cha ntchito yako; madalitso ndi chuma zidzakhala zako. 3 Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako. 4 Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa amene amaopa Yehova. 5 Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni masiku onse a moyo wako; uwone zokoma za Yerusalemu, 6 ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israeli. |
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
Biblica, Inc.