Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 40:5 - Buku Lopatulika

5 Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Inu Chauta, Mulungu wanga, mwatichitira zodabwitsa zambiri, mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo. Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu. Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo, sindingathe kuziŵerenga zonse chifukwa cha kuchuluka kwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Zambiri, Yehova Mulungu wanga, ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita. Zinthu zimene munazikonzera ife palibe amene angathe kukuwerengerani. Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera, zidzakhala zambiri kuzifotokoza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 40:5
14 Mawu Ofanana  

Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?


amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.


Wochita zazikulu zosasanthulika, ndi zodabwitsa zosawerengeka.


Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu; pakuti chifundo chake nchosatha.


Kudziwa ichi kundiposa ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako.


Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.


Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.


Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova, zolingalira zanu nzozama ndithu.


Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima.


Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?


Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa