Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 40:6 - Buku Lopatulika

6 Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapempha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Simudafune nsembe ndi zopereka, koma mwandipatsa makutu oti ndizimvera. Simudapemphe nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna, koma makutu anga mwawatsekula; zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo Inu simunazipemphe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 40:6
19 Mawu Ofanana  

pamenepo atsegula makutu a anthu, nakomera chizindikiro chilangizo chao;


amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.


Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri!


Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu.


Sindikudzudzula iwe chifukwa cha nsembe zako; popeza nsembe zako zopsereza zili pamaso panga chikhalire.


Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda.


Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.


pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake am'boole khutu lake ndi lisungulo; ndipo iye azimgwirira ntchito masiku onse.


Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde.


Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.


Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.


Koma mukadadziwa nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; simukadaweruza olakwa iwo osachimwa,


Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadze kudzaitana olungama, koma ochimwa.


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa