Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 1:3 - Buku Lopatulika

3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu.

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 1:3
39 Mawu Ofanana  

ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.


m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mau anga.


Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.


Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.


Ndipo pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, naona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisraele.


Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.


Yehova, ali mu Ziyoni, akudalitseni; ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.


Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.


Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa.


Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo;


pomwepo iye anamlandira Iye m'manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati,


Tsiku lomwelo mudzazindikira kuti ndili Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.


kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine.


Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.


chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina.


kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.


Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;


Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.


Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,


Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.


Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.


kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko.


kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;


imene anachititsa mwa Khristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, namkhazikitsa padzanja lake lamanja m'zakumwamba,


ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Khristu Yesu;


kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,


Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.


ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.


amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.


Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za mu Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.


Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa