Mawu a Mulungu m’Masalimo 5:4 amati, “Pakuti Inu simuli Mulungu wokondwera ndi zoipa; woipa sadzakhala nanu pamodzi.” Ndipo ndikukulimbikitsani kuti muzindikire kufunika koŵerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu, chifukwa ndiwo chitsogozo chathu cha tsiku ndi tsiku. Ngati tikufuna moyo wabwino, tiyenera kutsatira malamulo ndi mawu amene Ambuye anatipatsa m’Baibulo.
Choncho, tisiye zoipa zonse zimene sizikondweretsa Mulungu. Tiwongolere mapazi athu ndikutsatira mawu ake kuti atitsogolere ku choonadi chake. Popeza iye amadana ndi zoipa, tiyesetse ndi mtima wonse kuti tichotse njira yachinyengo mwa ife. Tibwerere kwa Mulungu ndikulapa machimo athu.
Chifundo chake chikufuna kutipulumutsa, kutiyeretse, ndikutibwezeretsa kuti tikakhale ndi moyo wabwino, wonga fungo lokoma pamaso pake.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:
Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa;
mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu;
mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.
Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.
Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa.
Pewapo, osapitamo; patukapo, nupitirire.
Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.
Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!
Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa mphulupulu siikhala ndi Inu.
Opusa sadzakhazikika pamaso panu, mudana nao onse akuchita zopanda pake.
Ndipo anati, Uyu ndi uchimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntovu wolemerawo pakamwa pake.
Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;
Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? Pakuti sasamba manja pakudya.
izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ai.
Thyolani mkono wa woipa; ndipo wochimwa, mutsate choipa chake kufikira simuchipezanso china.
anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;
wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,
akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,
opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo;
amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.
Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima; koma akuchita zoipa adzaonongeka.
Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa.
Wolungama sadzachotsedwa konse; koma oipa sadzakhalabe m'dziko.
Choipa chanu chikhoza kuipira munthu wonga inu, ndi chilungamo chanu chikhoza kukomera wobadwa ndi munthu.
Ndipo anawabwezera zopanda pake zao, nadzawaononga m'choipa chao; Yehova Mulungu wathu adzawaononga.
Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.
Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; inde, udzayang'anira mbuto yake, nudzapeza palibe.
Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka.
Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano.
Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza.
Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira.
Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe, ndipo mauta ao adzathyoledwa.
Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri.
Pakuti manja a oipa adzathyoledwa, koma Yehova achirikiza olungama.
Yehova adziwa masiku a anthu angwiro; ndipo cholowa chao chidzakhala chosatha.
Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta.
Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi.
Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.
Koma ukachenjeza woipa, osabwerera iye kuleka choipa chake kapena njira yake yoipa, adzafa mu mphulupulu yake; koma iwe walanditsa moyo wako.
koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva.
Ndipo Mombolo adzafika ku Ziyoni, ndi kwa iwo amene atembenuka kusiya kulakwa mwa Yakobo, ati Yehova.
Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.
Pakuti manja anu adetsedwa ndi mwazi, ndi zala zanu ndi mphulupulu, milomo yanu yanena zonama, lilime lanu lilankhula moipa.
Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.
Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.
Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa,
Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu.
kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,
njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.
Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.
Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro,
mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.
Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.
Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.
Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa;
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo:
kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,
osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,
achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;
akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.
Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.
Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?
Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova, moyo wanga ukadakhala kuli chete.
Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika.
iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.
Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.
Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma.
Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa.
Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa; ngakhale kuchitira nsanje amphulupulu.
pakuti mtima wao ulingalira za chionongeko; milomo yao ilankhula za mphulupulu.
Pakuti woipayo sadzalandira mphotho; nyali ya amphulupulu idzazima.
Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo, kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama.
Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika.
woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.
Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.
Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,
ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu; amayenda ndi m'kamwa mokhota.
Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake, amalankhula ndi zala zake;
zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu.
Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.
Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.
Yehova mu Mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.
Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima; palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense.
Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao padziko lapansi.
Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.
Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.
Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.
Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro; kapena kugwiriziza ochita zoipa.
Koma adzadzaza m'kamwa mwako ndi kuseka, ndi milomo yako kufuula.
Iwo akudana nawe adzavala manyazi; ndi hema wa oipa adzakhala kuli zii.
Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa;
Makala amoto awagwere; aponyedwe kumoto; m'maenje ozama, kuti asaukenso.
Munthu wamlomo sadzakhazikika padziko lapansi; choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse.
Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi.
Indedi, olungama adzayamika dzina lanu; oongoka mtima adzakhala pamaso panu.
amene adzipanga zoipa mumtima mwao; masiku onse amemeza nkhondo.
Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosachimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi chipasuko zili m'njira mwao.
Njira ya mtendere saidziwa, ndipo palibe chiweruziro m'mayendedwe mwao; akhotetsa njira zao; aliyense ayenda m'menemo sadziwa mtendere.
Usachitire nsanje anthu oipa, ngakhale kufuna kukhala nao;
Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.
Omwe atengedwa kuti akafe, uwapulumutse; omwe ati aphedwe, usaleke kuwalanditsa.
Ukanena, Taonani, sitinadziwe chimenechi; kodi woyesa mitima sachizindikira ichi? Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa? Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa machitidwe ake?
Mwananga, idya uchi pakuti ngwabwino, ndi chisa chake chitsekemera m'kamwa mwako.
Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako; ngati waipeza padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.
Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo.
Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso; koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.
Usakondwere pakugwa mdani wako; mtima wako usasekere pokhumudwa iye;
kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa, ndi kuleka kumkwiyira.
Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa; ngakhale kuchitira nsanje amphulupulu.
pakuti mtima wao ulingalira za chionongeko; milomo yao ilankhula za mphulupulu.
Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake.
Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziwa Inu; ndi chilungamo chanu pa oongoka mtima.
Phazi la akudzikuza lisandifikire ine, ndi dzanja la oipa lisandichotse.
Pomwepo padagwera ochita zopanda pake. Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso.
Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.
Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga, waleka kuzindikira ndi kuchita bwino.
Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho.
Wakuda mnzake amanyenga ndi milomo yake; koma akundika chinyengo m'kati mwake.
Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
Angakhale abisa udani wake pochenjera, koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.
Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.
Mtima wopulukira udzandichokera; sindidzadziwana naye woipa.
Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa;
phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.
Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:
Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.
Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.
Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.
Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.
Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.
Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu.
Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ake.
Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.
Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.
Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.
Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu:
koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga.
Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.
kukupulumutsa kunjira yoipa, kwa anthu onena zokhota;
akusiya mayendedwe olungama, akayende m'njira za mdima;
omwe asangalala pochita zoipa, nakondwera ndi zokhota zoipa;
amene apotoza njira zao, nakhotetsa mayendedwe ao.
Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.
Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.
Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao.
Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi chitsulo; onsewa achita movunda;
Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa;
iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.
Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake:
ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;
monga kwalembedwa, Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi;
palibe mmodzi wakudziwitsa, palibe mmodzi wakulondola Mulungu;
onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pake; palibe mmodzi wakuchita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu.
Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.
Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.
Yense wonyada mtima anyansa Yehova; zoonadi sadzapulumuka chilango.
Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.
Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?
Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.
Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.
Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m'manja mwa oipa.
Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa.
Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.
Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.
Wolingalira zakuchita zoipa anthu adzamtcha wachiwembu.
Maganizo opusa ndiwo tchimo; wonyoza anyansa anthu.
Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda.
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.
Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,
Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhale nalo dothi lakuya.
nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
amene alungamitsa woipa pa chokometsera mlandu, nachotsera wolungama chilungamo chake!
Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.
Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo;
ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.
Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa.
Kufatsa mtima ndi osauka kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.