Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


104 Mau a m'Baibulo Pa Nkhani

104 Mau a m'Baibulo Pa Nkhani

Buku la Aefeso limandiphunzitsa kuti ndisamanene mawu alionse oipa, koma mawu anga onse akhale opatsa mphamvu kwa anthu ondizungulira, kuti ndiwadalitse pamavuto alionse amene akukumana nawo.

Lilime langa linalengedwa kuti likhale chitoliro cha madalitso chimene Mulungu amafuna kugwiritsa ntchito pofalitsa uthenga ndi kumanga anthu ambiri. Ndiye chifukwa chake, ndikofunikira kwambiri kuchotsa chilichonse chimene sichichokera kwa Mulungu ndipo sichithandiza pakumanga.

Ndiyenera kusamala kwambiri ndi mawu anga, chifukwa ndidzaweruzidwa malinga ndi zimene ndimanena. Ndiyenera kukhala wofulumira kudalitsa m'malo motemberera mnzanga kapena kufalitsa miseche, chifukwa miseche siyabwino pamaso pa Mulungu.

Ndiyenera kuyesetsa kukhala wolankhula wamawu a Mulungu mwachangu, kuti chisomo chake ndi chifundo chake zikhale nane nthawi zonse. Ndikumbukire kusunga lilime langa ku zoipa ndi milomo yanga kuti isanene bodza, chifukwa munthu woipa amabweretsa ndewu zoopsa, koma woteteza mnzake amapulumutsa moyo.




Miyambo 11:13

Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; koma wokhulupirika mtima abisa mau.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:28

Munthu wokhota amautsa makani; kazitape afetsa ubwenzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:29

Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:16

Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:9

Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:11

Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:13

Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:19

Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi; usadudukire woyasama milomo yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 15:2-3

Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake. Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1

Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:20

Posowa nkhuni moto ungozima; ndi popanda kazitape makangano angoleka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:8

Mau akazitape akunga zakudya zolongosoka, zotsikira m'kati mwa mimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 141:3

Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:2

asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36

Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:1

Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:5-6

Kotero lilimenso lili chiwalo chaching'ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri! Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:11

Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:26

Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:4

kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:29-30

anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani; wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi, akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa: Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu; mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:23

Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake asunga moyo wake kumavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:13

Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:16

Usamnamizire mnzako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 15:1-3

Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika? Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake. Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:19

Pochuluka mau zolakwa sizisoweka; koma wokhala chete achita mwanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 41:6

Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza; mumtima mwake adzisonkhera zopanda pake, akanka nayenda namakanena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:27

Munthu wopanda pake akonzeratu zoipa; ndipo m'milomo mwake muli moto wopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:8

Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:15

Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:31

Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:18

Wobisa udani ali ndi milomo yonama; wonena ugogodi ndiye chitsiru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:1

Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:11

ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:9

Wobisa cholakwa afunitsa chikondano; koma wobwerezabwereza mau afetsa ubwenzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:22

Mau a kazitape ndi zakudya zolongosoka zitsikira m'kati mwa mimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:18

Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31-32

Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:5

Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:20

Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:10

Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:24

Mau okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m'moyo ndi olamitsa mafupa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 4:6

Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:28

Lilime lonama lida omwewo linawasautsa; ndipo m'kamwa mosyasyalika mungoononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:9

Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:20

Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:3

Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati chidzalalikidwa pa matsindwi a nyumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:23

Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 52:2-4

Lilime lako likupanga zoipa; likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga. Ukonda choipa koposa chokoma; ndi bodza koposa kunena chilungamo, ukonda mau onse akuononga, lilime lachinyengo, iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4-7

Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:14-15

Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungaonongane.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:18

Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:21

Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:13

Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:23

M'ntchito zonse muli phindu; koma kulankhulalankhula kungopatsa umphawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1-2

Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri. Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka. Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:20

Kodi uona munthu wansontho m'mau ake? Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:11

Mwa ichi chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:37

Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:2

Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:3

Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake; koma woyasamula milomo yake adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:2-3

ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; Koma inu simunaphunzire Khristu chotero, ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu; kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi. Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake. Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndiponso musampatse malo mdierekezi. Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa. Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva. ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:20

Ukhala, nuneneza mbale wako; usinjirira mwana wa mai wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:10

Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chili chokwanitsa lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:18-19

Monga woyaluka woponya nsakali, mivi, ndi imfa, momwemo wonyenga mnzake ndi kuti, ndi kusewera kumeneku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:2

Wina akutume, si m'kamwa mwako ai; mlendo, si milomo ya iwe wekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:13

Wobwezera mau asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:9

Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:28

Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe; koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:34

Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:22

Milomo yonama inyansa Yehova; koma ochita ntheradi amsekeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:14-15

Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:2

Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:16

Koma pewa nkhani zopanda pake; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:24

Tasiya m'kamwa mokhota, uike patali milomo yopotoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:15

Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:14

Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:18

Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:7

Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:22

koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 64:2-3

Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa; pa phokoso la ochita zopanda pake. Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:45

Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:28

Usachitire mnzako umboni womtsutsa opanda chifukwa; kodi udzanyenga ndi milomo yako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:9

musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:1-2

Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:5

Mboni yokhulupirika siidzanama; koma mboni yonyenga imalankhula zonama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:18-20

Monga woyaluka woponya nsakali, mivi, ndi imfa, momwemo wonyenga mnzake ndi kuti, ndi kusewera kumeneku. Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira. Posowa nkhuni moto ungozima; ndi popanda kazitape makangano angoleka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:34-35

Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:12-13

Lankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu. Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:5

Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa; wolankhula mabodza sadzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:16

Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:4

iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:18

Wochitira mnzake umboni wonama ndiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga, Wamkulukulu woyenera kutamandidwa, ndikukutamandani chifukwa cha chifundo chanu chachikulu ndi kukoma mtima kwanu kosatha. Palibe tsiku limene simusonyeza kukhulupirika kwanu pa moyo wanga. Mumadziwa zoyenda zanga zonse, kuyambira m'mawa mpaka usiku. Ndikukupemphani tsopano, Ambuye, kuti mufufuze mtima wanga. Ngati mupeza njira yolakwika mwa ine, ndikhululukireni. Ndisambitseni ku zoipa zanga ndi kundikonza. Sindikufuna kuti mawu oipa atuluke pakamwa panga, koma ndikufuna kulankhula choonadi chanu. Ndilanditseni ku chinyengo chilichonse. Sindikufuna kukhala munthu wopanda chifundo kwa mnzanga. Ndithandizeni kusunga ulemu wa m'bale wanga ndi kupewa miseche, chifukwa ndikudziwa kuti simukukondwera nazo. Ikani moto woyera pakamwa panga kuti muchotse chodetsa chilichonse, chifukwa ndikufuna kukhala chotengera cholemekezeka m'manja mwanu. Ndikupempha kuti nthawi zonse ndikatsegula pakamwa panga, ndikhale kudalitsa miyoyo ya ena. Zikomo chifukwa cha zonse, Yesu wokondedwa wanga. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa