Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 19:16 - Buku Lopatulika

16 Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Musamangoyendayenda uku ndi uku kumachita ukazitape pakati pa anthu a mtundu wanu. Musachite kanthu kalikonse kamene kangathe kudzetsa imfa ya munthu wina. Ine ndine Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “ ‘Musamapite uku ndi uku kunena bodza pakati pa anthu anu. “ ‘Musachite kanthu kalikonse kamene kangadzetse imfa kwa mnzanu. Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 19:16
24 Mawu Ofanana  

Iye wakupereka mabwenzi ake ku ukapolo, m'maso mwa ana ake mudzada.


Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.


Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.


Ukhala, nuneneza mbale wako; usinjirira mwana wa mai wako.


Usamnamizire mnzako.


Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.


Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.


Wobisa udani ali ndi milomo yonama; wonena ugogodi ndiye chitsiru.


Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; koma wokhulupirika mtima abisa mau.


Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi; usadudukire woyasama milomo yake.


Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi chitsulo; onsewa achita movunda;


Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.


Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.


nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha.


Wotembereredwa iye wakulandira chamwazi chakuti akanthe munthu wosachimwa. Ndi anthu onse anene, Amen.


Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse.


osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,


Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;


Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,


Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa