Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 5:22 - Buku Lopatulika

22 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:22
93 Mawu Ofanana  

Ndipo abale ake anaona kuti atate wake anamkonda iye koposa abale ake onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.


Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake.


Ndipo anatero Simei pakutukwana, Choka, choka, munthu wa mwazi iwe, woipa iwe;


Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi!


Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wake, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.


Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m'kaidi; pakuti adapsa naye mtima chifukwa cha ichi. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.


Naika oweruza m'dziko, m'mizinda yonse yamalinga ya mu Yuda, mzinda ndi mzinda;


Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena.


Ndipo anandizinga ndi mau a udani, nalimbana nane kopanda chifukwa.


Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.


Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi; adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa.


Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.


Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo; usavutike mtima ungachite choipa.


Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.


Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.


ngati ndambwezera choipa iye woyanjana ndine; (inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda chifukwa);


Munthu wopulukira sachidziwa; ndi munthu wopusa sachizindikira ichi;


Wanzeru amaopa nasiya zoipa; koma wopusa amanyada osatekeseka.


Milomo ya wopusa ifikitsa makangano; ndipo m'kamwa mwake muputa kukwapulidwa.


Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.


Ondida opanda chifukwa anandiinga ngati mbalame;


Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi mu ukali wake, anawauza abwere nao Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.


Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anasandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.


Chifukwa cha chiwawa unamchitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka kunthawi yonse.


Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka chikhakha tsiku lakupsinjika.


Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;


Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.


Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi?


Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.


Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa Gehena woposa inu kawiri.


Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa Gehena?


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula Kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu;


koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu;


Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeze.


Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.


Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.


Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao,


Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.


Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.


Khamu la anthu linayankha, Muli ndi chiwanda: afuna ndani kukuphani Inu?


Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?


Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.


Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu a milandu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.


Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu a milandu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.


Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza chosalungama chotani, poimirira ine pamaso pabwalo la akulu a milandu,


Koma pamene anawalamulira iwo achoke m'bwalo la akulu a milandu, ananena wina ndi mnzake,


Ndipo atamva ichi, analowa mu Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa a bwalo la akulu a milandu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo.


Ndipo m'mene adadza nao, anawaika pabwalo la akulu a milandu. Ndipo anawafunsa mkulu wa ansembe,


Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu a milandu,


Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.


Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israele, Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.


M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;


kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.


koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira?


Popeza waumphawi salekana m'dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.


Mudziikire oweruza ndi akapitao m'midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama.


asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni.


asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.


Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;


ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;


Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe?


Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.


amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;


osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.


Iye amene anena kuti ali m'kuunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino.


M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.


Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.


Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbike mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.


Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa