Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 5:23 - Buku Lopatulika

23 Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako paguwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 “Nchifukwa chake ngati wabwera ndi chopereka chako ku guwa, nthaŵi yomweyo nkukumbukira kuti mnzako wina ali nawe nkanthu,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 “Nʼchifukwa chake, pamene ukupereka chopereka chako pa guwa lansembe ndipo nthawi yomweyo ukumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa,

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:23
17 Mawu Ofanana  

Pamenepo wopereka chikho wamkulu anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zochimwa zanga lero.


Tsono mfumu inanenanso ndi Simei, Udziwa iwe choipa chonse mtima wako umadziwacho, chimene udachitira Davide atate wanga; chifukwa chake Yehova adzakubwezera choipa chako pamutu pako mwini.


Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine.


kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.


Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.


Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?


usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.


Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.


Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.


Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa