Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 34:13 - Buku Lopatulika

13 Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa, pakamwa pako pasakambe zonyenga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 34:13
22 Mawu Ofanana  

Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu, ndi kulola mau otere atuluke m'kamwa mwako.


Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga.


Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.


M'kati mwake muli kusakaza, chiwawa ndi chinyengo sizichoka m'makwalala ake.


Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi.


Milomo yonama inyansa Yehova; koma ochita ntheradi amsekeretsa.


Oipa amagwa kuli zii; koma banja la olungama limaimabe.


Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake; koma woyasamula milomo yake adzaonongeka.


Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake.


Mboni yonama sidzapulumuka chilango; wolankhula mabodza adzaonongeka.


Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake asunga moyo wake kumavuto.


Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangachite monyenga; chomwecho Iye anali Mpulumutsi wao.


Funani chokoma, si choipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wa makamu adzakhala ndi inu, monga munena.


musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,


Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.


Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.


Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.


Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,


amene sanachite tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa