Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 13:3 - Buku Lopatulika

3 Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake; koma woyasamula milomo yake adzaonongeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake; koma woyasamula milomo yake adzaonongeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Amene amagwira pakamwa pake amasunga moyo wake, koma amene amangolakatika amaonongeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iye amene amagwira pakamwa pake amateteza moyo wake, koma amene amayankhula zopanda pake adzawonongeka.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 13:3
18 Mawu Ofanana  

Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga.


Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo.


Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.


Anzeru akundika zomwe adziwa; koma m'kamwa mwa chitsiru muononga tsopano lino.


Pochuluka mau zolakwa sizisoweka; koma wokhala chete achita mwanzeru.


Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo; koma chitsiru cholongolola chidzagwa.


M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa; koma wolungama amatuluka m'mavuto.


Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu; koma moyo wa akhama udzalemera.


M'kamwa mwa chitsiru muli nthyole ya kudzikuza; koma milomo ya anzeru idzawasunga.


Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake.


M'kamwa mwa wopusa mumuononga, milomo yake ikhala msampha wa moyo wake.


Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi; usadudukire woyasama milomo yake.


Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake asunga moyo wake kumavuto.


Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.


Nanena naye, Akandimangitsa nazo zingwe zatsopano, zosagwira nazo ntchito pamenepo ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina.


Pomwepo anamfotokozera mtima wake wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndine Mnaziri wa Mulungu chiyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandichokera, ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina aliyense.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa