2 Akorinto 12:20 - Buku Lopatulika20 Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Pakuti ndikuona kuti pamene ndibwera sindidzakupezani monga mmene ndikufunira kuti muzikhalira, ndipo simungadzandione monga mmene mukufunira kundionera. Ndikuopa kuti pangadzakhale mkangano, nsanje, kupserana mitima, kugawikana, ugogodi, miseche, kudzitukumula ndi chisokonezo. Onani mutuwo |