Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 12:21 - Buku Lopatulika

21 kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ndikuwopa kuti ndikadzabweranso kwanuko, mwina Mulungu wanga nkudzandinyazitsa pamaso panu, ineyo nkudzalira misozi chifukwa cha ambiri amene adachimwa kale, ndipo sadalape zonyansa zao, dama lao, ndi mayendedwe ao oipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ndikuopa kuti pamene ndidzabwerenso, Mulungu adzandichepetsa pamaso panu, ndipo ndidzamva chisoni ndi ambiri amene anachimwa kale ndipo sanalape zonyansa, zachigololo ndi zilakolako zoyipa zimene anachita.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 12:21
37 Mawu Ofanana  

Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu.


Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba chovala changa, ndi malaya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndevu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa.


Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Ndipo Mose anabwerera kunka kwa Yehova, nati, Ha! Pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolide.


Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.


kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.


Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.


ndi kukhala okonzeka kubwezera chilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.


Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.


Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;


Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.


Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa,


Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a chipangano anali m'manja mwanga.


Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova masiku makumi anai usana ndi usiku ndinagwa pansiwa; popeza Yehova adati kuti adzakuonongani.


Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;


Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;


koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane naonso malaya ochitidwa mawanga ndi thupi.


Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.


Iye wakuchitira umboni izi, anena, Indetu; ndidza msanga. Amen; idzani, Ambuye Yesu.


Ndipo Samuele sanadzenso kudzaona Saulo kufikira tsiku la imfa yake; koma Samuele analira chifukwa cha Saulo; ndipo Yehova anali ndi chisoni kuti anamlonga Saulo mfumu ya Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa