Mtima wanga, dziwani kuti dyera ndi chinthu chomwe chimatigwira tonse, mosasamala kanthu za msinkhu wathu, kapena kuti ndife ndani.
M’Baibulo, muli nkhani zambiri zomwe zimatithandiza kuzindikira kuopsa kwa dyera. M’buku la Mlaliki, Mfumu Solomoni inalankhula za kufupika kwa moyo ndi kupanda pake kwa chuma ndi ulemerero wa dziko lapansi. Iye amatilimbikitsa kuyika chiyembekezo chathu mwa Mulungu, chifukwa zonse zomwe tili nazo ndi zomwe tinakwanitsa zidzatha.
Yesu, m’Chipangano Chatsopano, anatiphunzitsa kufunika koika maganizo athu pa zinthu zosatha, osati kufuna kuvomerezedwa ndi anthu. Mawu ake amatipatsa njira yopezera cholinga chenicheni cha moyo wathu, moyo wodzaza ndi chikondi cha Mulungu ndi cha anansi athu.
Dyera limatiletsa kukhala odzichepetsa ndipo limatipangitsa kufuna kudzikweza tokha, kuiwala chikondi ndi chifuniro cha Mulungu. Tiyeni tichenjere zimenezi.
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa; koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.
Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.
Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.
Chifukwa chake chotsani zopweteka m'mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa chabe.
Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;
Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.
Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.
Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti? Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?
chifukwa cha machimo onse a Baasa, ndi machimo a Ela mwana wake anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele ndi zachabe zao.
Monga chipini chagolide m'mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.
Ndipo anakaniza malemba ake, ndi chipangano anachichita ndi makolo ao, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asachite monga iwowa.
Ndinyansidwa nao moyo wanga; sindidzakhala ndi moyo chikhalire; mundileke; pakuti masiku anga ndi achabe.
Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Asatame zopanda pake, kudzinyenga nazo; pakuti zopanda pake zidzakhala chombwezera chake.
Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.
Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu; pakuti sitinatenge kanthu polowa m'dziko lapansi, ndiponso sitingathe kupita nako kanthu pochoka pano;
Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.
Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake; koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.
Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.
amene pakamwa pao alankhula zachabe, ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
Ndilanditseni ndi kundipulumutsa kudzanja la alendo, amene pakamwa pao alankhula zachabe, ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.
Mau a wina ati, Fuula. Ndipo ndinati, Kodi ndifuule chiyani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo; udzu unyala, duwa lifota; chifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu. Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire.
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.
Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.
Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.
Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu.
Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.
Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zachabe, ndi tchimo ngati ndi chingwe cha galeta;
Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.
amene apalamulitsa munthu mlandu, namtchera msampha iye amene adzudzula pachipata, nambweza wolungama ndi chinthu chachabe.
Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa; koma Mau a Ambuye akhala chikhalire. Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo.
Taonani, inu muli achabe, ndi ntchito yanu yachabe; wonyansa ali iye amene asankha inu.
Taona, iwo onse, ntchito zao zikhala zopanda pake ndi zachabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo.
Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.
Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele.
Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe. mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo; Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m'fumbi ndi onse abweranso kufumbi.
Pakuti miyambo ya anthu ili yachabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, ntchito ya manja a mmisiri ndi nkhwangwa.
Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?
Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa; osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako, koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa.
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitire ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamike; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira. Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;
Monga anatuluka m'mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m'dzanja lake.
Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu; alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi chuma chambiri.
Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake?
atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe?
inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.
Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.
Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.
Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.
Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.
Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao, odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao;
Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.
Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao. Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire, ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo; atchapo dzina lao padziko pao. Koma munthu wa ulemu wake sakhalitsa, afanana ndi nyama zakuthengo, afanana nazo.
Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,
Pamene pakufuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzachotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala nacho cholowa m'phiri langa lopatulika.
Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye; pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka.
Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji? Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?
Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.
Chifukwa chake kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao; achivala chiwawa ngati malaya. Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao, malingaliro a mitima yao asefukira.
Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Khristu. Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,
Pali chinthu chachabe chimachitidwa pansi pano; chakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera ntchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera ntchito za olungama. Ndinati, Ichinso ndi chabe. Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m'vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano.
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake. Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa mu ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.
popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.
Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake; pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse; ulemu wake sutsika naye kumtsata m'mbuyo.
Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati fumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono. Ndipo Lebanoni sakwanira kutentha, ngakhale nyama zake sizikwanira nsembe yopsereza. Amitundu onse ali chabe pamaso pa Iye; awayesa ngati chinthu chachabe, ndi chopanda pake.
Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake.
mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili padziko lapansi m'chilakolako.
Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.
Koma ndinati, Ndagwira ntchito mwachabe, ndatha mphamvu zanga pachabe, ndi mopanda pake; koma ndithu chiweruziro changa chili ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.
Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.
Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;
Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Ichinso ndi chabe ndi chosautsa mtima.
Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.
Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso.
Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.