Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 12:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Kenaka Iye anawawuza kuti, “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 12:15
34 Mawu Ofanana  

Ndipo Simei ananyamuka, namangirira mbereko pabulu wake, nanka ku Gati kwa Akisi kukafuna akapolo ake; namuka Simei, nabwera nao akapolo ake kuchokera ku Gati.


Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.


Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.


Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri.


Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.


Zapang'ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.


Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?


Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa; koma yemwe ada chisiriro adzatanimphitsa moyo wake.


Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga.


Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.


Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.


Tsoka iye wakupindulitsira nyumba yake phindu loipa, kuti aike chisanja chake ponyamuka, kuti alanditsidwe m'dzanja la choipa!


zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:


Ndipo Iye ananena nao fanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino.


Koma Afarisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka.


Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;


Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.


kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.


Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;


Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,


Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.


pamene ndinaona pazofunkha malaya abwino a ku Babiloni, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi chikute chagolide, kulemera kwake masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pakepo.


okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;


Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa