Mlaliki 2:17 - Buku Lopatulika17 Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Motero moyo wanga ndidaipidwa nawo, chifukwa chakuti zonse zochitika pansi pano zimandimvetsa chisoni. Ndithudi, zonsezo nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Kotero ndinadana nawo moyo chifukwa ntchito zimene zimagwiridwa pansi pano ndi zosautsa kwa ine. Ntchito zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe. Onani mutuwo |