Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 5:7 - Buku Lopatulika

7 Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Maloto akachuluka pamachulukanso zokamba zachabechabe. Koma iwe uzilemekeza Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Maloto ochuluka ndi mawu ochuluka ndi zinthu zopandapake. Kotero lemekeza Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 5:7
11 Mawu Ofanana  

Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


Ndidziwa kuti zonse Mulungu azichita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kuchotsapo; Mulungu nazichita kuti anthu akaope pamaso pake.


Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.


Pakuti loto lafika mwakuchuluka ntchito; ndipo mau a chitsiru mwakuchuluka maneno.


Kuli kwabwino kugwira ichi; indetu, usachotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzatuluka monsemo.


Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino;


koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu.


Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzake pomlamulira.


Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa