Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 5:6 - Buku Lopatulika

6 Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pakamwa pako pasakuchimwitse, kuti choncho usayenerenso kukauza wansembe wa Mulungu kuti, “Ai, ndinkangonena!” Chifukwa chiyani ufuna kuputa Mulungu? Kodi ukufuna kuti aononge zimene wazigwirira ntchito?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pakamwa pako pasakuchimwitse. Ndipo usanene kwa mthenga wa mʼNyumba ya Mulungu kuti, “Ndinalakwitsa polumbira.” Chifukwa chiyani ukufuna Mulungu akwiye ndi mawu ako ndiponso ntchito ya manja ako?

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 5:6
23 Mawu Ofanana  

mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.


Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse.


Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga chisomo; koma milomo ya chitsiru idzachimeza.


Ndidziwa kuti zonse Mulungu azichita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kuchotsapo; Mulungu nazichita kuti anthu akaope pamaso pake.


Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;


Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;


Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.


Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala.


koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo.


Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Khristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankho.


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.


Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.


Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa