Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 2:15 - Buku Lopatulika

15 Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Kani zimene zimagwera chitsiru nanenso zidzandigwera zomwezo! Nanga tsono ineyo nzeru zambiri chotere nzanji?” Pamenepo ndidaona kuti zimenezinso nzopanda phindu!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Pamenepo ndinalingalira mu mtima mwanga, “Zochitikira chitsiru zidzandichitikiranso ine. Nanga tsono phindu langa nʼchiyani pakukhala wanzeru?” Ndinati mu mtima mwanga, “Ichinso ndi chopandapake.”

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 2:15
9 Mawu Ofanana  

taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso.


Pakuti m'nzeru yambiri muli chisoni chambiri; ndi yemwe aenjezera chidziwitso aenjezera zowawa.


Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe.


Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu.


Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji?


Pakuti wanzeru ali ndi chiyani choposa chitsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pamaso pa amoyo ali ndi chiyani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa