Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 4:16 - Buku Lopatulika

16 Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Ichinso ndi chabe ndi chosautsa mtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Ichinso ndi chabe nichisautsa mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Mfumu ikhoza kulamulira anthu osaŵerengeka, komabe itamwalira, palibe aliyense amene adzayamikire zomwe mfumuyo idachita. Ndithudi, zimenezinso nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mfumu ikhoza kulamulira anthu osawerengeka, komabe itamwalira, palibe amene adzayamikire zomwe mfumuyo inachita. Izinso ndi zopandapake, nʼkungozivuta chabe.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 4:16
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.


Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukulu, kotero kuti pansi panang'ambika ndi phokoso lao.


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.


Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, wachiwiri, amene adzalowa m'malo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa