Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 16:7 - Buku Lopatulika

7 Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma Chauta adauza Samuele kuti, “Usayang'ane maonekedwe ake, ngakhale kutalika kwa msinkhu wake, poti ndamkana ameneyo. Chauta sapenya monga m'mene apenyera anthu. Anthu amapenya zakunja, koma Chauta amapenya zamumtima.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Koma Yehova anati kwa Samueli, “Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 16:7
34 Mawu Ofanana  

koma sanayang'anire Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, ndipo nkhope yake inagwa.


Ndipo mu Israele monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pamutu wake mwa iye munalibe chilema.


Ndipo Davide adzaonjezanso kunenanso ndi Inu? Pakuti mudziwa mnyamata wanu, Yehova Mulungu.


pamenepo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kuchita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zake zonse, amene Inu mumdziwa mtima wake, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;


Anenenjinso Davide kwa inu za ulemu wochitikira mtumiki wanu? Pakuti mudziwa mtumiki wanu.


Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.


Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.


pamenepo mumvere mu Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera aliyense monga mwa njira zake zonse, monga mudziwa mtima wake; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu;


Muli nao maso a thupi kodi? Mupenya kodi monga umo apenyera munthu?


Yang'anani kumwamba, nimuone, tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu.


Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.


Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.


Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova; koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?


Njira zonse za munthu ziyera pamaso pake; koma Yehova ayesa mizimu.


Ukanena, Taonani, sitinadziwe chimenechi; kodi woyesa mitima sachizindikira ichi? Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa? Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa machitidwe ake?


Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.


Koma, Yehova wa makamu, amene aweruza molungama, amene ayesa impso ndi mtima, ndikuoneni Inu mulikuwabwezera chilango, pakuti kwa Inu ndawulula mlandu wanga.


Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.


Koma, Inu Yehova wa makamu, amene muyesa olungama, amene muona impso ndi mtima, mundionetse ine kubwezera chilango kwanu pa iwo; pakuti kwa inu ndaululira mlandu wanga.


Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.


Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.


Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu.


Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,


Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.


Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife.


Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.


amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu,


koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.


Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.


Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu.


Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu ena onse anamlekeza m'chifuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa