Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 62:9 - Buku Lopatulika

9 Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu akulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Anthu otsika ndi mpweya chabe, ngakhale anthu okwera ndi nthunzi chabe, onsewo ndi oluluka pa sikelo, ndi opepuka kupambana mpweya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Anthu wamba ndi mpweya chabe; anthu apamwamba ndi bodza chabe; ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe; iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 62:9
25 Mawu Ofanana  

Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.


Abisalomu anachitira zotero Aisraele onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wao; chomwecho Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israele.


Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.


Pofulumizidwa mtima ndinati ine, anthu onse nga mabodza.


Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira akulu.


Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.


Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.


Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.


Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.


Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri; koma Inu ndinu pothawira panga polimba.


Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.


Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati fumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono.


Amitundu onse ali chabe pamaso pa Iye; awayesa ngati chinthu chachabe, ndi chopanda pake.


TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera.


Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!


Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.


Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndipo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa, Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu, ndi kuti mukapambane m'mene muweruzidwa.


Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndili mkazi wa mtima wachisoni; sindinamwe vinyo kapena chakumwa chowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.


Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe.


Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuimba kwao, nati, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani.


Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa