Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 39:5 - Buku Lopatulika

5 Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Onani, mwandipatsa masiku ochepa chabe, nthaŵi ya moyo wanga siili kanthu pamaso panu. Ndithudi, munthu aliyense ndi mpweya chabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri, kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu; moyo wa munthu aliyense ndi waufupi. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 39:5
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.


Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kunka ku Yerusalemu?


Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba, apitirira opanda chiyembekezo.


Munthu akunga mpweya; masiku ake akunga mthunzi wopitirira.


Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.


Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.


Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi; munalengeranji ana onse a anthu kwachabe?


Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero, kuti tikhale nao mtima wanzeru.


Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe.


Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.


Amitundu onse ali chabe pamaso pa Iye; awayesa ngati chinthu chachabe, ndi chopanda pake.


inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.


Koma ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa