Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 23:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo amene aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 23:12
15 Mawu Ofanana  

Anthu akakugwetsa pansi, udzati, Adzandikweza; ndipo adzapulumutsa wodzichepetsayo.


Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza amdziwira kutali.


Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.


Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.


Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.


Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.


Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.


Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.


Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.


Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.


Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa