Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 4:4 - Buku Lopatulika

4 Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono ndidazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 4:4
19 Mawu Ofanana  

ndipo anali ndi chuma cha nkhosa, ndi chuma cha zoweta, ndi banja lalikulu: ndipo Afilisti anamchitira iye nsanje.


Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse.


Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka; koma ndani angalakike ndi nsanje?


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.


Pakuti pali munthu wina agwira ntchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lake kwa munthu amene sanagwirepo ntchito. Ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu.


Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Ichinso ndi chabe ndi chosautsa mtima.


Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji?


Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru.


Ndipo makolo aakuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,


Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?


osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa