Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 144:4 - Buku Lopatulika

4 Munthu akunga mpweya; masiku ake akunga mthunzi wopitirira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Munthu akunga mpweya; masiku ake akunga mthunzi wopitirira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Munthu ali ngati mpweya, masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Munthu ali ngati mpweya; masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 144:4
16 Mawu Ofanana  

Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.


Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.


kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi, amene kuzika kwao kuli m'fumbi, angothudzulidwa ngati njenjete.


Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu, popeza masiku athu a padziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;


Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu.


Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.


Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.


Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.


Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi; munalengeranji ana onse a anthu kwachabe?


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe.


Chabe zachabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi chabe.


koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa