Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 12:8 - Buku Lopatulika

8 Chabe zachabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chabe zachabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Nkuwonatu Mlaliki akuti, “Zonse nzopanda phindu. Ndithudi, zonse nzopandapake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Zopanda phindu! Zopandapake!” akutero Mlaliki. “Zonse ndi zopandapake!”

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 12:8
10 Mawu Ofanana  

Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.


Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya mu Yerusalemu.


Ine Mlaliki ndinali mfumu ya Israele mu Yerusalemu.


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.


Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe.


Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?


Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udyo sudzapulumutsa akuzolowerana nao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa