Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 2:11 - Buku Lopatulika

11 Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono ndidayamba kulingalira zonse zimene ndidazichita, ntchito zolemetsa zonse zimene ndidazigwira, nkuwona kuti zonsezo zinali zopanda phindu. Kunali kungodzivuta chabe. Ndithu panalibe choti nkupindulapo pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga, ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze, zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe, palibe chomwe ndinapindula pansi pano.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 2:11
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.


Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi; munalengeranji ana onse a anthu kwachabe?


Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.


Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani?


Wogwira Ntchito aona phindu lanji m'chomsautsacho?


Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.


Ichinso ndi choipa chowawa, chakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa chabe adzaona phindu lanji?


Taonani, sichichokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto ntchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pake?


Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa