Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 2:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo chilichonse maso anga anachifuna sindinawamane; sindinakanize mtima wanga chimwemwe chilichonse pakuti mtima wanga unakondwera ndi ntchito zanga zonse; gawo langa la m'ntchito zanga zonse ndi limeneli.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo chilichonse maso anga anachifuna sindinawamana; sindinakaniza mtima wanga chimwemwe chilichonse pakuti mtima wanga unakondwera ndi ntchito zanga zonse; gawo langa la m'ntchito zanga zonse ndi limeneli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chilichonse chimene maso anga ankachilakalaka, ndidaachitenga. Mtima wanga sindidaumane zokondweretsazo, pakuti mtima wangawo unkakondwa ndi ntchito zanga zonse zolemetsa. Zimenezi zinali mphotho ya ntchito zanga zolemetsazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna; mtima wanga sindinawumane zokondweretsa. Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse, ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 2:10
21 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso.


kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.


Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?


Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.


Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera.


Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.


Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.


Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.


Pakuti munthu ali ndi chiyani m'ntchito zake zonse, ndi m'kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno?


Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m'ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.


M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo?


Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.


Inde masiku ake onse amadya mumdima, ndipo zimchulukira chisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.


Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.


munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa.


Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m'vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano.


Chikondi chao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kalikonse kachitidwe pansi pano.


Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.


Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.


Nakwera iye, nauza atate wake ndi amai wake, nati, Ndapenya mkazi mu Timna wa ana aakazi a Afilisti; ndipo tsono munditengere uyu akhale mkazi wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa