Zekariya 5 - Buku LopatulikaMasomphenya achisanu ndi chimodzi: mpukutu wouluka 1 Pamenepo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, taonani, mpukutu wouluka. 2 Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinayankha, Ndiona mpukutu wouluka; utali wake mikono makumi awiri, ndi chitando chake mikono khumi. 3 Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lilikutulukira padziko lonse; pakuti aliyense wakuba adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi aliyense wakulumbira zonama adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili. 4 Ndidzalitulutsa ili, ati Yehova wa makamu, ndipo lidzalowa m'nyumba ya wakuba, ndi m'nyumba ya iye wolumbira monama pa dzina langa; ndipo lidzakhala pakati pa nyumba yake, ndi kuitha pamodzi ndi mitengo yake ndi miyala yake. Masomphenya achisanu ndi chiwiri: mkazi ndi efa 5 Pamenepo mthenga wakulankhula ndi ine anatuluka, nati kwa ine, Kwezatu maso ako, nuone ngati nchiyani ichi chilikutulukachi. 6 Ndipo ndinati, Nchiyani ichi? Nati iye, Ichi ndi efa alikutuluka. Natinso, Ichi ndi maonekedwe ao m'dziko lonse; 7 ndipo taonani, chozunguniza chantovu chotukulidwa: ndipo ichi ndi mkazi wokhala pakati pa efa. 8 Ndipo anati, Uyu ndi uchimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntovu wolemerawo pakamwa pake. 9 Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a chumba, nanyamula efayo pakati padziko ndi thambo. 10 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Amenewa amuka naye kuti efayo? 11 Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike efayo, namkhazikeko pamalo kwake. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi