Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 5:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo anati, Uyu ndi uchimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntovu wolemerawo pakamwa pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo anati, Uyu ndi uchimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntovu wolemerawo pakamwa pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mngeloyo adati, “Ameneyu akutanthauza kuipa konse.” Atatero adakankhira mkaziyo m'gondolo muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mngeloyo anati, “Chimenechi ndi choyipa,” ndipo anamukankhira mkaziyo mʼdengu muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 5:8
11 Mawu Ofanana  

Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.


Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga; ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.


Zoipa zakezake zidzagwira woipa; adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.


Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake; zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvu yanga; Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwagonjetsa.


Ndiye Mkanani, m'dzanja lake muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa.


Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga;


Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga?


ndipo taonani, chozunguniza chantovu chotukulidwa: ndipo ichi ndi mkazi wokhala pakati pa efa.


Dzazani inu muyeso wa makolo anu.


natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza machimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa