Zekariya 5:9 - Buku Lopatulika9 Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a chumba, nanyamula efayo pakati padziko ndi thambo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a chumba, nanyamula efayo pakati pa dziko ndi thambo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Nditayang'ananso, ndidaona akazi aŵiri okhala ndi mapiko onga a kakoŵa. Akaziwo ankabwera chouluka ndi mphepo. Adanyamula gondolo lija, kupita nalo pakati pa dziko lapansi ndi mlengalenga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona akazi awiri akuwuluka kubwera kumene kunali ine; akuwuluzika ndi mphepo. Iwo anali ndi mapiko ngati a kakowa, ndipo ananyamula dengu lija, kupita nalo pakati pa mlengalenga ndi dziko lapansi. Onani mutuwo |