Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 5:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike efayo, namkhazikeko pamalo kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike efayo, namkhazikeko pa malo kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Akupita nalo ku dziko la Sinara kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzakhazikamo gondololo pa phaka lake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Iye anayankha kuti, “Ku dziko la Babuloni kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzayikamo dengulo.”

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 5:11
10 Mawu Ofanana  

Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.


Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum'mawa, anapeza chigwa m'dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko.


Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu,


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.


popeza watitumizira mau ku Babiloni, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zao?


Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Amenewa amuka naye kuti efayo?


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


Yehova adzachita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwitsa, miliri yaikulu ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa