Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 6:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pamene Chauta adaona kuti anthu a pa dziko lapansi aipa koopsa, ndiponso kuti mitima yao inali yodzaza ndi maganizo oipa,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pamene Yehova anaona kuti kuyipa kwa munthu pa dziko lapansi kunali kwakukulu ndi kuti nthawi zonse amalingalira ndi kukhumbira kuchita zoyipa zokhazokha,

Onani mutuwo Koperani




Genesis 6:5
24 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.


Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, wakumwa chosalungama ngati madzi.


Udzasunga kodi njira yakale, anaiponda anthu amphulupulu?


Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.


mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu;


Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.


Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.


Ndipo anati kwa ine, Lowa, kapenye zonyansa zoipa alikuzichita komweko.


Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;


Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa Munthu.


Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa