Ukunena sikuli bwino konse. Pamaso pa Mulungu, kunena bodza n’koipa ndipo kumabweretsa mavuto aakulu kwa amene akuchita zimenezi akapezeka. Usaname pothawa udindo wako kapena kuti ukondweretse munthu wina, chifukwa kunena bodza kumakupanga munthu wosakhulupirika.
Ukamabodza, umadziwa bwino zomwe ukuchita, ndipo ngati chikumbumtima chako sichikukuvutitsa, ndiye kuti waopa Mulungu ndipo wazolowela bodza. Ngati ukhoza kunena bodza ukuyang’ana munthu m’maso, uli pa njira yolakwika, osati chifukwa cha zimene ukuchitira munthuyo, koma chifukwa chakuti suganizira momwe Mulungu amakuonera.
Munthu akayamba kunena bodza, amakhala munthu wopanda komanso wozizira. Poyamba ungaganize kuti kunena bodza kamodzi sikuli koipa kwenikweni, koma ukabwerezanso ukuchita kutsegula khomo, ndipo ukazindikira, zidzakhala mochedwa, sungathe kusiya ndipo watsegula chibowo chachikulu. Bodza lingakulekanitse ndi Mulungu ndikupangitsa kuti utayitse mabwenzi ofunika komanso maubwenzi.
Wabodza amadzinyenga yekha, akutaya ulemu, kuyamikiridwa ndi chitetezo. Tsopano popeza wadziwa zonsezi, samala ndi mawu otuluka pakamwa pako ndipo usakhale kapolo wa mizimu yoipa yomwe ikufuna kuti usanene zoona. Bodza limakhala msampha womwe ungatulukemo pokhapokha ngati wavomereza machimo ako kwa Khristu, kutaya zoipa ndi kukhala ndi mtima wowona nthawi zonse.
Kunena bodza kumakulekanitsa ndi Mulungu, usadziloŵetse m’moyo wopanda kukhalapo kwake. Ulipobe nthawi yoti uwongolere njira yako ndikuchita zoyenera.
Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.
Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.
Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?
achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;
Wakuchita chinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga; wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.
Mlomo wangwiro suyenera chitsiru; ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa: Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu; mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.
Otsala a Israele sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.
ndipo oweruza afunsitse bwino; ndipo taonani, mboniyo ikakhala mboni yonama, yomnamizira mbale wake; mumchitire monga iye anayesa kumchitira mbale wake; motero muchotse choipacho pakati panu.
Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.
M'mero mwao muli manda apululu; ndi lilime lao amanyenga; ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao; m'kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa;
Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.
Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo;
Lilime lako likupanga zoipa; likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga. Ukonda choipa koposa chokoma; ndi bodza koposa kunena chilungamo, ukonda mau onse akuononga, lilime lachinyengo, iwe.
Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m'zipata zanu;
Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi. Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda.
Mudzaononga iwo akunena bodza; munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.
anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;
Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;
Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;
Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;
Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.
Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.
Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.
Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye; Ndipo pamene Yesu anali mu Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate, koma sanaupeze zingakhale mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pake anadza awiri,
koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.
Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro; mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro. Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.
ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?
Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:
Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.
m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olochedwa m'chikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo chamoto;
Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.
Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi;
Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m'chosalungama chao;
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.
Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo, ndi nkhosa zinai pa nkhosayo.
Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake. Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.
Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukakamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?
Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,
Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.
ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima.
Chifukwa chake ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israele, yense monga mwa njira zake, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.
Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi? Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa. Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama. Indedi, pali Mulungu wakuweruza padziko lapansi. Inde, mumtima muchita zosalungama; padziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu.
Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.
Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima; ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,
Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.
Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula, momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga.
Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa.
Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo; ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.
Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro; mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.
Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera, Ndipo si chotero chokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isaki; pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo, chotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono. Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau. Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai. Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni. Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo. Pakuti lembo linena kwa Farao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe padziko lonse lapansi. Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima. Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza chifuniro chake? kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka. Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero? Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi? Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko? Ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene Iye anazikonzeratu kuulemerero, ndi ife amenenso Iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu? Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhale anthu anga, ndidzawatcha anthu anga; ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa. Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo, Simuli anthu anga ai, pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo. Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala monga mchenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka. Pakuti Ambuye adzachita mau ake padziko lapansi, kuwatsiriza mwachidule. Ndipo monga Yesaya anati kale, Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyire ife mbeu, tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora. Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;
Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.
Waumphawi woyenda mwangwiro apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.
Sindinakulembereni chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi.
Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.
Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.
Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika.
Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.
Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika? Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake.