Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 78:36 - Buku Lopatulika

36 Koma anamsyasyalika pakamwa pao, namnamiza ndi lilime lao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Koma anamsyasyalika pakamwa pao, namnamiza ndi lilime lao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Koma iwo adamthyasika ndi pakamwa pao, adamnamiza ndi lilime lao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo, kumunamiza ndi malilime awo;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:36
11 Mawu Ofanana  

Pakumva m'khutu za ine adzandimvera, alendo adzandigonjera monyenga.


Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kuchita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhale chete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiope Ine konse?


Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.


Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.


Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.


Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito.


Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zake, adzambwezera monga mwa machitidwe ake.


Pakuti anthu ake olemera adzala ndi chiwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limachita monyenga m'kamwa mwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa