Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Yohane 2:4 - Buku Lopatulika

4 Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Munthu akamanena kuti, “Ine ndimadziwa Mulungu,” koma samvera malamulo a Mulunguyo, ndi wabodza ameneyo ndipo mwa iye mulibe choonadi.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 2:4
13 Mawu Ofanana  

Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.


Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo akumdulidwe,


Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.


Tikanena kuti sitidachimwe, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ake sakhala mwa ife.


Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi;


Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi.


Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake.


Iye amene anena kuti ali m'kuunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino.


Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuone Iye, ndipo sanamdziwe Iye.


Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.


Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa