Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 4:2 - Buku Lopatulika

2 koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbu mtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Takaniratu njira zonse zochititsa manyazi zimene anthu amatsata mobisika. Sitichita kanthu monyenga kapena kupotoza mau a Mulungu; koma pakulankhula zoona poyera pamaso pa Mulungu, tifuna kuti anthu onse ativomereze m'mitima mwao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Koma ife takaniratu njira zonse zachinsinsi ndi zochititsa manyazi. Sitichita kanthu mwachinyengo kapena mopotoza Mawu a Mulungu. Mʼmalo mwake, timayankhula choonadi poyera pamaso pa Mulungu, kufuna kuti aliyense ativomereze mu mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 4:2
16 Mawu Ofanana  

Nati, Bwerezaninso kawiri; nabwerezanso. Nati, Bwerezani katatu; nabwereza katatu.


Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.


Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.


Ndipo ndingakhale ndili wosaphunzira m'manenedwe, koma sinditero m'chidziwitso, koma m'zonse tachionetsa kwa inu mwa anthu onse.


Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.


Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtima zanu.


mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga osocheretsa, angakhale ali oona;


Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.


Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;


pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa