Yohane 8:44 - Buku Lopatulika44 Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201444 Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa44 Inu ndinu ana a Satana. Iye ndiye tate wanu, ndipo mukufuna kumachita zimene tate wanuyo amalakalaka. Iye uja chikhalire ngwopha anthu. Sadakhazikike m'zoona, chifukwa mwa iye mulibe zoona. Kunena bodza ndiye khalidwe lake, pakuti ngwabodza, nkukhalanso chimake cha mabodza onse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero44 Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza. Onani mutuwo |