Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:3 - Buku Lopatulika

3 Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma Petro adamufunsa kuti, “Iwe Ananiya, chifukwa chiyani walola mtima wako kugwidwa ndi Satana mpaka kumanamiza Mzimu Woyera pakupatula ndalama zina za munda wako?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama?

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:3
25 Mawu Ofanana  

Ndipo ukuti, Adziwa chiyani Mulungu? Aweruza kodi mwa mdima wa bii?


Kunena mwansontho, Ichi nchopatulika, kuli msampha kwa munthu, ndi kusinkhasinkha pambuyo pake atawinda.


Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho.


Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?


Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.


Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.


Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m'kamwa mwake.


Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.


Ndipo Satana analowa mwa Yudasi wonenedwa Iskariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo.


Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,


Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.


anagulitsa chao, napatula pa mtengo wake, mkazi yemwe anadziwa, natenga chotsala, nachiika pa mapazi a atumwi.


Pamene unali nao, sunali wako kodi? Ndipo pamene unagulitsa sunali m'manja mwako kodi? Bwanji chinalowa ichi mumtima mwako? Sunanyenga anthu, komatu Mulungu.


Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.


Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako.


Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.


Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa