Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 58:3 - Buku Lopatulika

3 Oipa achita chilendo chibadwire, asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Oipa achita chilendo chibadwire, asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Anthu oipa ndi osokera kuyambira ali m'mimba mwa mai ao, anthu amabodza ndi otayika kuyambira tsiku la kubadwa kwao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera; kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 58:3
9 Mawu Ofanana  

Munthu nchiyani kuti akhale woyera, wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?


Chibadwire ine anandisiyira Inu, kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.


Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.


Izizo ziuzungulira pa malinga ake usana ndi usiku; ndipo m'kati mwake muli zopanda pake ndi chovuta.


Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.


Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israele, amene ndakunyamulani kuyambira m'mimba, ndi kukusenzani chibadwire;


Inde, iwe sunamve; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire.


Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.


amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa