Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 58:4 - Buku Lopatulika

4 Ululu wao ukunga wa njoka; akunga mphiri yogontha m'khutu, itseka m'khutu mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ululu wao ukunga wa njoka; akunga mphiri yogontha m'khutu, itseka m'khutu mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ali ndi ululu wonga wa njoka, ali ngati mphiri yogontha, imene yatseka makutu ake,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka, ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 58:4
14 Mawu Ofanana  

Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m'mundamu tidye.


Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


koma chakudya chake chidzasandulika m'matumbo mwake, chidzakhala ndulu ya mphiri m'kati mwake.


Adzayamwa ndulu ya mphiri; pakamwa pa njoka padzamupha.


Anola lilime lao ngati njoka; pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.


Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.


Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m'funkha la mphiri.


Pakuti, taonani, ndidzatumiza pa inu njoka, mphiri, zosalola kuitanidwa; ndipo zidzakulumani inu, ati Yehova.


Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa Gehena?


Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?


M'mero mwao muli manda apululu; ndi lilime lao amanyenga; ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;


Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka, ndi ululu waukali wa mphiri.


koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa