Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 58:2 - Buku Lopatulika

2 Inde, mumtima muchita zosalungama; padziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Inde, mumtima muchita zosalungama; pa dziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iyai, mitima yanu imangolingalira zoipa, kuweruza kwanu kosalungama kumadzetsa chiwawa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama, ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 58:2
14 Mawu Ofanana  

Pakuti anakupangirani choipa, anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita.


Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu.


Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo?


Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.


Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu;


Njira ya wolungama ili njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.


Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.


Akalonga ake m'kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.


Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa