Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 23:28 - Buku Lopatulika

28 Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Inunso muli chimodzimodzi: pamaso pa anthu mumaoneka olungama, pamene m'kati mwanu m'modzaza ndi chiphamaso ndi zoipa zina.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Chimodzimodzinso, kunja mumaoneka kwa anthu kuti ndinu olungama koma mʼkatimo ndinu odzaza ndi chinyengo ndi zoyipa zina.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 23:28
13 Mawu Ofanana  

Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo; ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.


Angakhale abisa udani wake pochenjera, koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.


Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.


Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama,


Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje,


Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.


Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.


Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa