1 Yohane 2:21 - Buku Lopatulika21 Sindinakulembereni chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Sindinakulemberani chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Ndakulemberani, osati chifukwa chakuti simudziŵa choona, koma chifukwa chakuti mumachidziŵa, ndipo mukudziŵanso kuti bodza silichokera ku choona. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Sindikukulemberani chifukwa choti simudziwa choonadi ayi, koma chifukwa choti mumadziwa choonadicho, ndipo mukudziwanso kuti bodza silichokera pa choonadi. Onani mutuwo |