Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Koma Isaki adayankha kuti, “Mng'ono wako anabwera, ndipo wandinyenga. Iyeyo ndiye amene watenga madalitso ako onse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Koma iye anati, “Mʼbale wako anabwera mwachinyengo ndipo watenga madalitso ako.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:35
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika.


Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikire iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji?


Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ake onse, asasowe mmodzi; pakuti ndili nayo nsembe yaikulu yochitira Baala; aliyense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Koma Yehu anachichita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.


Kodi munenera Mulungu mosalungama, ndi kumnenera Iye monyenga?


Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.


Kodi sitili naye Atate mmodzi ife tonse? Sanatilenge kodi Mulungu mmodzi? Tichita monyengezana yense ndi mnzake chifukwa ninji, ndi kuipsa chipangano cha makolo athu?


Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;


asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa