Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:36 - Buku Lopatulika

36 Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungire ine mdalitso?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungira ine mdalitso?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Pamenepo Esau adati, “Kameneka nkachiŵiri kundichenjeretsa iye uja. Nchosadodometsa kuti dzina lake ndi Yakobe. Ukulu wanga wauchisamba adandilanda, ndipo tsopano wandilandanso madalitso anga. Kodi monga madalitsowo simudandisungireko ndi pang'ono pomwe?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:36
4 Mawu Ofanana  

Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwake ndipo dzanja lake linagwira chitendeni cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isaki anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo.


Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.


Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa